Instructions to candidates
Do not open this examination paper until instructed to do so.
Answer one essay question only. You must base your answer on at least two of the part 3
works you have studied and compare and contrast these works in response to the question.
Answers which are not based on a discussion of at least two part 3 works will not score
high marks.
You are not permitted to bring copies of the works you have studied into the examination room.
The maximum mark for this examination paper is [25 marks].
2216 – 0524
3 pages/páginas © International Baccalaureate Organization 2016
–2– M16/1/AXCHW/SP2/NYA/TZ0/XX
Yankhani funso limodzi lokha la chimangirizo. Onetsetsani kuti mu yankho lanu mwafotokozamo
zokhudza mabuku osachepera awiri a m’Gulu 3 omwe munawerenga ndipo mufananitse ndi
kusiyanitsa nkhanizi mu yankho lanu. Mayankho amene sakambako za mabuku osachepera awiri a
mu Gawo 3 simudzalandira nawo malikisi ochuluka.
Masewero
2. “Mathero (mapeto) a sewero ndiofunikira ngati momwe pachimake pa sewero palinso pofunikira.”
Kodi mawuwa ndi owona bwanji malinga ndi masewero osachepera awiri amene munawerenga?
Ndakatulo
5. Pogwiritsa ntchito ndakatulo zimene zinalembedwa ndi anthu osachepera awiri zimene
munawerenga fananitsani (yerekezani) momwe anasonyezera maganizo a anthu amene
akuyankhula mu ndakatulozo.
6. Fananitsani (yerekezani) njira zomwe alembi a ndakataulo osachepera awiri amene munawerenga
anagwiritsa ntchito pofuna kupereka maphunziro kwa owerenga.
Nkhani zopeka
7. Fotokozani luso lomwe alembi a nkhani zopeka zosachepera ziwiri zimene munawerenga
akugwiritsa ntchito pofuna kusiyanitsa pakati pa amtengambali aamuna ndi aakazi.
8. Fotokozani momwe alembi osachepera awiri a nkhani zopeka zimene munawerenga anagwiritsira
malo ndi nthawi yochitikira nkhani pofuna kutisonyeza chikhalidwe cha anthu.
Nkhani zosapeka
10. Fotokozani zipangizo za munkhani zimene zagwiritsidwa ntchito pofuna kusonyeza makhalidwe
mu nkhani zosapeka zosachepera ziwiri zimene munawerenga.
11. Alembi a nkhani zosapeka amagwiritsa ntchito mawu odziwika bwino komanso osadziwika
bwino pofuna kukwaniritsa zolinag zina zake munkhaniyo. Fananitsani momwe kayankhulidwe
kanagwiritsidwira ntchito ndi zotsitira zake munkhani zosapeka zosachepera ziwiri zimene
munawerenga.